"ANYAMATA AMAMENYERA CHIPSERA MTIMA MU CHIGAWO CHOYAMBA" - MSUKWA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Silver Strikers Mapopa Msukwa wati timu yake inavutika kwambiri mchigawo choyamba chifukwa anyamata ake anapsa mtima kuti achinye zigoli zambiri koma atawadekhetsa anasewera bwino mchigawo chachiwiri.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa Karonga United 4-1 kuti ibwenzere chipongwe chimene analandira sabata yatha atagonja 3-0 kuti atulutsidwe mu chikho cha Airtel Top 8.
Timuyi inakanika kupeza chigoli mu chigawo choyamba chomwe chinatha 0-0 koma mchigawo chachiwiri, anamwetsa zigoli zitatu motsogozana kuti apheretu masewerowa.
Msukwa wati sanali ndi cholinga cha kubwenzera koma kusewera kuti apambane ndi kutenga mapoints atatu.
"Mchigawo choyamba amamenyera chipsera mtima nde tinawauza kuti masewero awa si ofuna zigoli zambiri, adekhe ndikumenya mpira wathu zomwe zinatithandiza kwambiri," iye anatero.
Chipambanochi chathandiza timu ya Silver kubwerera pa nambala yachiwiri
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores