mwi
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
KAYIRA WACHOKA KU LIBERTY
Mphunzitsi watimu ya Liberty FC, Chimango Kayira, walengeza kuti watula pansi pa udindo wake.
Iye wati wapanga chiganizochi kamba koti samagwira ntchito yake mwa ufulu kamba koti ena amalowerera pa ntchito ndi ziganizo zake.
Iye wati ndi wokondwa kuti wathandizira timuyi mochuluka komanso kuti anabweretsa ndi kuthandizira osewera mu kaseweredwe kawo ndipi wathokoza akuluakulu a timuyi.
Wosewera wakale wa FCB Nyasa Big Bullets, ESCOM United komanso timu ya dziko linoyu sanafotokoze chitsogolo cha ntchito yake.
FAM YAPEPESA KWA MFUMU YAKU LILONGWE
Bungwe loyendetsa mpira mu dziko lino la Football Association of Malawi latulutsa kalata yopepesa kwa mfumu ya mzinda wa Lilongwe, a Peter Banda, kamba kokanizidwa kukapereka nawo mphoto kwa osewera pamathero a chikho cha NBS Bank Charity Shield.
Izi zadza patangodutsa maola ochepa unduna wa achinyamata, chikhalidwe ndi masewero komanso mtsogoleri wa bungwe la ma khonsolo mdziko muno, a Isaac Jomo Osman, anauza FAM kuti ipepese.
Bungweli lati silinachite kukonza kuti lichitire chipongwe mfumuyi koma ena omwe amayendetsa zinthu pa bwalo pomwepo anaona kuti zinthu zina zisokonekera malingana ndi momwe anakonzera.
Iwo ati akufufuza momwe zinthu zonse zinayendera kuti apeze chenicheni chimene chinachitika pa mwambowu.
Tipepese kuti panali kusintha kwa mmene gemu ya Mamelodi Sundowns vs Esperance ya Loweruka pa 18 April imene inathera 1-0 koma poyamba tinaika molakwika kuti inatherka 0-0. Kusinthaku kwasintha omwe ali ap top 3 kuchoka pa olosera 13 kufika pa 9. Pano tatumiza ndalama kwa olosera 9 omwe apambana.
Choncho tikupepesa kwa olosera 4 omwe anali pa top 3 poyamba koma pano achoka.
Mtsogoleri wa Malawi Local Government Association, Isaac Jomo Osman, wati bungwe la Football Association of Malawi lipepese pasanathe maola 24 pa zomwe zinachitikira mfumu ya mzinda wa Lilongwe, a Peter Banda.
A Banda analetsedwa kukapereka nawo mphoto kwa osewera amatimu a Mighty Wanderers komanso FCB Nyasa Big Bullets pomwe masewero amu Charity Shield anatha.
A Osman ndi achiwiri kuyankhulapo pa nkhaniyi pomwe unduna wa zamasewero watulutsa kale kalata koma khonsolo ya mzinda wa Lilongwe sinayankhule kalikonse.
GWENGWE'S BRACE SECURES POOLE TOWN'S PLAYOFFS PLACE
Malawian England based forward Shaquille Gwengwe scored twice as Poole Town beat Havant & W 2-0 in the Southern League Premier South to secure promotion playoffs in England on Saturday.
Gwengwe took his tally to 40 League goals in his first season with the team proving his brilliance and heroics for the team as he leads with four goals in the golden boot race with a game to go.
Meanwhile, the victory has sealed a fourth place in the League for Poole Town as they have 74 points from 41 games.
The team will face either Gloucester City or Farnham Town depending on who finishes third in the League in search of a promotion in the National League South League.
UNDUNA WA ZAMASEWERO WAUZA FAM KUTI IPEPESE
Unduna wa achinyamata, chikhalidwe ndi masewero wadzudzula zomwe zinachitika pa masewero amu chikho cha Charity Shield pomwe mfumu ya mzinda wa Lilongwe, a khansala Peter Banda, analetsedwa kukapereka nawo mphoto pakutha pa masewerowa.
Mu kalata yomwe yasainidwa ndi mlembi wamkulu, Jeremiah Ndalama, yati ndi yokhumudwa ndi mchitidwewu ndipo yapempha Football Association of Malawi ipepese kamba ka mchitidwewu.
Undunawu watinso FAM ilembe lipoti pa chifukwa chenicheni chomwe mfumuyi inakanizidwira kufika pa malo operekera mphotozi komanso kuti apereke chilango kwa onse okhudziwa.
A Banda analetsedwa kukapereka mphoto kwa matimu a Mighty Wanderers ndi FCB Nyasa Big Bullets omwe anakumana pa masewerowa ati kamba koti anavala zovala zosiyana ndi ena omwe anakapereka mphotozi.
Timu ya Wanderers ndi yomwe inali akatswiri a chikhochi kutsatira kupambana 1-0 ndi chigoli cha Sama Thierry Tanjong.