NKHANI
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets ikulingalira zokambirana ndi katswiri wawo wakale, Babatunde Adepoju, kuti abwerere kutimuyi kutsatira kuti mgwirizano wake ukutha posachedwa ndi timu ya Venda FC yaku South Africa.
Babatunde wakhala wosewera wofunika kwambiri ku timuyi mu nthawi yomwe wakhala akutumikira timuyi ndipo wayithandiza kupambana zikho zosiyanasiyana.
Malingana ndi malipoti a Twaha Chimuka, katswiriyu ali mdziko momwe muno kutsatira kutha kwa ligi yachiwiri yaku South Africa koma mgwirizano wake ukutha mwezi wa mawa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores