Malawi yatuluka ku COSAFA ya atsikana
Timu ya Malawi ya atsikana osapyola zaka 20 yatuluka mu mpikisano wa COSAFA Women's Championship kutsatira kugonja 6-3 ndi timu ya Zimbabwe lachiwiri masana.
Timuyi imatsalira 3-1 pakutha pa chigawo choyamba koma inabwenza mchigawo chachiwiri komabe Zimbabwe inamwetsa zina zitatu kuti ipambane masewerowa,
Mphunzitsi watimuyi, Linda Kasenda, wati atsikana ake sanasewere bwino pomwe amakanika kupatsirana ndi kutchinga kumbuyo zomwe ndi zokhumudwitsa.
"Mpikisano wonsewu tikanatha kuchita bwino koma atsikana sanayikirepo mtima zomwe zativuta kwambiri." Anatero Kasenda.
Timuyi yamaliza pansi penipeni pa gulu lawo pomwe yapeza point imodzi pa masewero atatu omwe agonja kawiri ndi kulepherana kamodzi
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores