SILVER YATULUKA KOYAMBA KUTALI NDI LILONGWE
Timu ya Silver Strikers ikusewera masewero awo oyamba kutali kwa mzinda wa Lilongwe pomwe akumane ndi timu ya Mighty Wanderers pa bwalo la Zomba lamulungu masana.
Timuyi inayamba ndi kukumana ndi Kamuzu Barracks ku Mponera pa bwalo la Champions asanalandire Moyale Barracks pakhomo kenako kuyendera Blue Eagles ku Civo ndipo anabwereranso pakhomo kulandira timu ya Masters FC.
Mphunzitsi watimuyi, Peter Mgangira wati bwalo la Zomba ndi labwino pansi pake ndipo akuyembekezera kukhala ndi masewero apamwamba patsikuli.
Iye wati mwa nthawi zonse samaopa timu iliyonse koma amangopereka ulemu Kwa omwe akusewera nawo ndipo akonzeka bwino pa masewerowa.
"Osewera akuchita kupikisana zomwe tikuchita kusowanso kuti tiyambitsa ndani koma takonzeka bwino ndithu. Tikukumana ndi timu yabwino yomwe ili ndi osewera abwino komanso aphunzitsi abwino koma ifeyo chomwe tikupitira ndi kuti tikachite bwino basi," Iye anatero.
Chipambano chikhala chopambana kwamb
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores