"ANYAMATA AMBIRI LERO SANALI BWINO" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Gilbert Chirwa, wati chabwino chimene timu yake inakwanitsa kuchita ndi kuletsa Red Lions kuti isagoletse koma anyamata ake sanasewere bwino.
Iye amayankhula atatha masewero omwe alepherana 0-0 ndi Red Lions kuti ataye mapoints awiri pakhomo mu masewerowa.
Iye wati zimakhala zovuta kuti osewera odalilika salibwino patsiku la masewero ndi chifukwa chake zawavuta.
"Tinayesera kulowetsako anyamata ena omwe anayesetsa komabe zinativuta, lero sitinali mu mpira ndipo zambiri zativuta kwambiri," anatero Chirwa.
Iye wati zofunika kukonza ndi zambiri ndipo timu singathe kuweruzidwa ndi masewero anayi okha ndipo nthawi yoti azitolere ndi yochuluka poti matimu enanso akutaya mapoints.
Timuyi yatsika kufika pa nambala yachinayi mu ligi pomwe ili ndi mapoints asanu ndi atatu pa masewero anayi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores