"Ndikudabwa kuti masapotawo amawaonera kuti osewerawa" - Mponda
Mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Peter Mponda, wati ndi odabwa ndi zoyankhula za masapota ena atimuyi kuti sanalowetse bwino osewera pomwe amasewera ndi Mighty Wanderers ati poti iyeyo ndi yemwe amakhala ndi osewerawo.
Iye amayankhula patsogolo pa maseweronso ena ndi Mighty Wanderers koma mu chikho cha FDH Bank omwe akubwera atagonja 3-0 ndi Manoma lamulungu lathali.
Iye wapempha ochemererawa kupewa kunyoza osewera akagonja masewero awo poti amakhala kuti anayikapo mtima koma zavuta.
"Osewerawa samazilowetsa okha koma amalowetsedwa ndi munthu nde ndi bwino aziloza chala yemwe amawalowetsa osewerawa yemwe ndi ine koma anyamata mu bwalo amayesetsa kuzipereka zimangokhala kuti tsiku lina sanadzuke bwino," anatero Mponda.
Patsogolo pa masewerowa, Iye wati timu yake ili ndi mwayi waukulu wokonza zinthu zomwe zinalakwika ndipo akudziwa kuti molalo ya Wanderers ili pamwamba koma akuyang'ana zokafika mu ndime
yotsiriza.
Iye watinso timu yake sisowa osewera aliyense pa masewerowa pomwe osewera onse alibwino bwino ndipo akhalanso ndi Yankho Singo pa masewerowa.
Opambana pa masewerowa adzazigulira malo mu ndime yotsiriza ya chikhochi ndipo adzakakumana ndi opambana pakati pa Silver Strikers ndi Civil Service United mu ndime yotsiriza.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores