"BULLETS NDIIMENE ILI NDI ADVANTAGE" - NYIRONGO
Katswiri olankhulirapo pankhani zamasewero m'dziko muno, Hamdan Nyirongo wati timu ya FCB Nyasa Big Bullets ndiimene ili ndi mwayi waukulu ofika mundime yotsiriza muchikho cha FDH Bank poyerekeza ndi timu ya Mighty Wanderers.
Iye amalankhula izi mu program ya nkhani zamasewero ya Sports Review pa kanema wa Luntha Lolemba.
Malingana ndi Nyirongo, timu ya Mighty Wanderers ilibe osewera akutsogolo abwino kotero zikupereka danga lalikulu kutimu ya Bullets kuti ikhoza kufika ndime yotsiliza mosavuta.
"Ku Bullets kuli ma striker ndi osewera pakati odziwa kuchinya pamene ku Wanderers kuja kulibe, ma striker awo ngakufa. Kwa Ine Bullets ndi Silver ndiomwe adzakumane mu final." Nyirongo anatero.
M'nzake Sebastien Liwonde anatsutsana naye pomwe anapereka mwayi kumatimu a Mighty Wanderers ndi Civil Service United kuti ndiamene afike ndime yotsiliza ya chikhochi.
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets inagonjetsa Kamuzu Barracks 2-1 Loweruka kuti ifi
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores