"Ngati wina wake anatipanga chipongwe atikhululukire" - Nkunika
Mphunzitsi watimu ya Jenda United wati tsopano akukanika kumvetsa chimene chikuvuta kutimuyi kuti igonje masewero onse amu NBS Bank National Division League mpaka wapempha kuti ngati anachitidwa chipongwe amwakhululukire.
Uchizi Nkunika amayankhula kutsatira kugonja 2-1 ndi timu ya Ndirande Stars lachiwiri ndipo wati zikusowetsa mtendere kuti timu ikumamenya bwino komabe kukanika kupambana.
"Nzovuta kukamba kwake chifukwa tikumenya chimodzimodzi koma osayenda. Ngati pali wina anatipanga chipongwe atikhululukire Koma ngati zili zakwa Mulungu tipambana ndipo matimu onse awa tidzawaswa." Anatero Nkunika.
Iye wanenetsa kuti timu yake situluka mu ligiyi ndipo chaka cha mawa iseweranso mu ligiyi koma wadandaula kuti oyimbira akuononga mpira kwambiri mu ligiyi.
Timuyi ili pa nambala 12 mu ligiyi opanda point iliyonse pomwe yagonja kasanu ndi kanayi mu ligiyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores