Timu ya Kukoma Ntopwa Queens yaikidwa mu gulu A la mpikisano wa COSAFA CAF Women's Championship pamodzi ndi matimu a Mamelodi Sundowns yaku South Africa, Beauties FC yaku Namibia ndi Ndola ZESCO Girls yaku Zambia.
Izi ndi malingana ndi mayere omwe bungwe la COSAFA linachititsa lachiwiri ku mmawa.
Aka ndi kachiwiri kuti timuyi ipite ku mpikisanowu poti inapitakonso mu chaka cha 2023 ndipo chaka chatha, Ascent Academy ndi imene idayimilira dziko lino ku mpikisano omwe unachitikira m'dziko mommuno.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores