"Jenda siyituluka mu ligi" - Nkunika
Mphunzitsi watimu ya Jenda United, Uchizi Nkunika, wanenetsa kuti timu yake situluka mu ligi ya NBS Bank National Division angakhale kuti agonja mmasewero asanu ndi amodzi omwe asewera mu ligiyi.
Iye anayankhulapo kutsatira kusachita bwino kwa timuyi yomwe sinapezeko point angakhale imodzi koma Iye wati timuyi imenyerabe nkhondo mpaka ipeze chipambano choyamba chomwe chitsegulire mwayi kutimuyi.
"Tilimbikirabe kuti mwina nkupezako chipambano choyamba zikatero ndekuti chikhala chiyambi cha zabwino. Sitituluka mu ligi, masewero akadalipo ochuluka ndipo tilimbikirabe mpaka tidzafike kumtundako." Anatero Nkunika.
Mphunzitsiyu watsogolera timuyi mu masewero awiri okha poti analowa mmalo mwa Obvious Banda yemwe anachotsedwa Kamba kosachita bwino mmasewero anayi.
Jenda yagonja ndi Bangwe All Stars, Mitundu Baptist, Namitete Zitha, FOMO FC, Ntaja United komanso Baka City ndipo ili pansi penipeni pa nambala 12 opanda point.
Wolemba : Hastings Wadza Kas
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores