Anthu ochuluka a dabwa ndi ganizo la aphunzitsi a timu ya dziko lino pomusiya katswiri womwetsa kutsogolo Binwell Katinji.
Katinji anatengedwa mochedwa mu m'bindikiro wa masewero a CHAN koma anagoletsako mu masewero onse awiri ndi Comoros.
Chomwe chadabwitsa anthu kwambiri ndi kuti omwetsa zigoli, Ephraim Kondowe, ndi yemwe wasankhidwa pamwamba pa Katinji ngakhale kuti Kondowe anavutika mmasewero ndi Comoros.
Izi ndi malingana ndi ndemanga za anthu ochuluka pa tsamba la mchezo la Facebook atawona ndandanda womwe aphunzitsiwa atulutsa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores