NKHANI
Bangwe All Stars yomwe yasewera mu ligi yaikulu ya dziko lino mu zaka za 2023 mpaka 2024 yathetsedwa.
Mwini wake watimuyi, Mphatso Jika, watsimikiza za nkhaniyi poyankhula ndi wayilesi ya MBC Radio 2 lachiwiri ku mmawa.
Iye wati chiganizochi chabwera kamba koti sangakwanitsenso kuthandiza timuyi pa nkhani ya za chuma poti amagwiritsa za mnthumba mwake.
Timuyi inalowa mu ligi yaikuluyi kuchokera ku ligi yaing'ono yakummwera mu chaka cha 2022 ndipo inathera pa nambala 6 mu chaka choyamba asanatuluke chaka chathachi.
Izi ndi chimodzimodzi matimu ngati a Sable Farming ndi Masters Security omwe anathetsedwa atangotuluka mu ligiyi.
Admin mwati tonse mwatitumizila ndalama zomwe tawina? Ine ndalama yanga sinafike koma nambala ndinatumiza kalekale. 0981658760.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores