NKHANI
Timu ya Civil Service United yasaina katswiri wakale wa Mighty Tigers, Precious Chiudza, yemwe wasaina mgwirizano wa zaka ziwiri ndi timuyi.
Chiudza ankayenera kupita ku Civil mu mwezi wa August koma mapepala ake anatulutsidwa mochedwa ndi Tigers kupangitsa kuti asasewerenso mpira mu chigawo chachiwiri cha ligi.
Iye wapita kutimuyi mwa ulere potinso mgwirizano wake omwe anali nawo ku Tigers watheratu.
Katswiriyu yemwe anapita ku Tigers mu 2019 ngati osewera kutsogolo akuyembekezeka kukasewera ngati wotseka kumbuyo chakumanzere kutimuyi kamba ka ukadaulo wake wokwanitsa kusewera malo omwe wapatsidwa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores