NKHANI
Komiti ya oyimbira ku bungwe la Football Association of Malawi latsiliza kuunikira dandaulo la timu ya Silver Strikers lomwe anapereka posagwirizana ndi ziganizo za oyimbira Mwayi Msungama pa masewero awo ndi FCB Nyasa Big Bullets.
Komitiyi yati penate yomwe Msungama anapereka komanso kukana chigoli chomwe a Silver akukhulupilira kuti chinalowa zinachitika molingana ndi malamulo a kayimbilidwe.
Zateremu zikuonetsa kuti Silver inafadi mwa mtima bii ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets 2-1 moyera mtima.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores