"Chipanda kutopa Wanderers sikanachinya" - Kaonga
Mphunzitsi watimu ya Songwe Border United, Edwin Kaonga, wati timu yake inachinyitsa zigoli nthawi yothaitha chifukwa choti osewera anatopa koma wayamikira osewera kuti anasewera bwino.
Iye amayankhula atatha masewero omwe anagonja 2-0 ndi timu ya Wanderers pomwe anakwanitsa mphindi 85 osachinyitsako chigoli pa masewerowa.
Kaonga anati timu yake inasewera bwino kwambiri ndipo kupanda kuti osewera ake sanatope Wanderers sikanapeza chigoli.
Iye watinso timu yake ilimbikirabe mu masewero atsalawa kuti mwina atha kutolako kenakake mu ligi.
"Masewero akadalipo ndithu ndipo ifeyo tizisewerabe moti sitingayankhule pano kuti tituluka kapena ayi. Tikuonetsabe dziko kuti sikuti ndife timu yoipa koma kuti zotsatira zimangotivutabe mwa tsoka basi," anatero Kaonga.
Timuyi yatsala ndi masewero asanu ndi atatu kuti itsilize onse ndipo yapambana kamodzi5, kulepherana kawiri ndi kugonja ka 19 kuti akhale ndi mapoints asanu okha pansi pa ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores