"AKACHEPEKEDWA ATIPEZA NDIPO TIWAYANKHA" - HAIYA
Mtsogoleri wa bungwe la Football Association of Malawi (FAM), Fleetwood Haiya wati kuchita bwino kwa timu ya Silver Strikers FC mu mpikisano wa CAF Champions League ndichinthu chonyadilitsa kwambiri kudziko lino.
A Haiya ati kupambana kwa timuyi pogonjetsa Young Africans 1-0 pabwalo la Bingu Loweruka zikutanthauza kuti Malawi ngati dziko yawinanso.
Polankhula pabwalo la Bingu atatha masewerowa, Haiya anathokoza boma la Malawi kudzera mwa nduna ya za m'dziko a Alfred Gangata pachidwi chimene anaonetsa pamasewerowa ndipo anati ali ndichikukhulupilira kuti izi zipitilira mtsogolomu.
Ndipo poyankha ngati bungweli litengepo gawo pothandizira otsatira timuyi kuti adzayipelekeze paulendo wa m'dziko la Tanzania kumasewero achibwereza, Haiya anayankha motere,
"Zimenezo tiasilire eni ake a timuyi. Ngati pali kuchepekedwa kapena kupempha kulikonse atipeza ndipo ifeyo tiwayankha moyenelera." Iye anatero.
Andrew Joseph anagoletsa chigoli chok
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores