"Masewero a lero atiwonetsa pomwe tikusowekera" - Kandulu
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Sullivan Kandulu, wayamikira timu ya FCB Nyasa Big Bullets Kamba kowagonjetsa pomwe wavomereza kuti timu yake inachita zolakwitsa zingapo zomwe zathandizira kuti agonje.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 0-2 pa bwalo la Chitipa kukhala kugonja koyamba patadutsa masewero asanu ndi anayi ndipo wati anachulutsa zolakwika mpake kugonja.
"Ukamasewera ndi matimu akulu-akulu mwina timantha timakhalapo nde chigoli choyamba kunali kulakwitsa kwambiri kumbuyo komanso timakanika kusunga mpira nde tivomereze kuti tagonja." Iye Anafotokoza.
Iye wati mavuto onse omwe anachita awaona ndipo ziwathandiza kuti awakonze kuti akamakumana ndi timu ya Silver Strikers mmasewero awo otsatira adzachite bwino.
Timuyi ili pa nambala 9 ndi ma points okwana 19 pomwe yapambana kanayi, kulepherana kasanu ndi kawiri ndi kugonja kasanu mu ligiyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores