"Mmutu mwa atsikana mukuyenda zaku South Africa" - Jomo
Mphunzitsi watimu ya Kukoma Ntopwa Queens, Isaac Jomo Osman, wati zinali zovuta kuti atsikana awo asewere mpira pakuti kaganizidwe kawo kali pa ulendo wopita m'dziko la South Africa.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 0-1 ndi timu ya Mighty Wanderers Women mu ligi ya NBM National Women's Premiership ndipo Iye wadandaula kuti samayenera kupatsidwa masewerowa.
"Anali masewero abwino kwambiri komabe zimatengera kaganizidwe ka osewera poti ife mmutu mwathu mukuyenda zaku South Africa komabe tiwayamikire kuti anayesetsabe kungoti tikakumana ndi Wanderers nthawi zonse timavutika." Anatero Jomo.
Iye watinso akukhulupilira kuti timu yake ilibwino patsogolo pa ulendowu ndipo tsopano akayesetsa kuti akachite bwino mu mpikisanowu.
Timuyi ikadali pa nambala yachiwiri mu ligi pomwe ili ndi ma points okwana asanu ndi anayi (9) pa masewero anayi omwe asewera mu ligiyi ndipo apambana katatu ndi kugonja kamodzi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores