Katswiri watimu ya Scorchers, Bernadette Mkandawire, wabwerera ku timu ya FCB Nyasa Big Bullets Women komwe wasaina mgwirizano wa ka nthawi kochepa.
Mkandawire anali mu dziko la Kazakhstan komwe amasewera mu timu ya BIIK Shymkent komwe anapitako mu mwezi wa December mu chaka cha 2024.
Iye anakwanitsa kugoletsa zigoli ziwiri mu ligi yomwe ikadaseweredwabe mdzikolo ndipo anapita pamodzi ndi Vanessa Chikupira ku timuyi.
Kubwera kwake kuthandize timu ya Bullets Women yomwe ikusewera mu ligi ya National Bank of Malawi National Women's Premiership..
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores