"Tinabwera kuti tidzapeze chipambano" - Ikwanga
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Kondwa Ikwanga, wati siwokhutira ndi kufanana mphamvu ndi timu ya Mighty Wanderers pomwe wati anakonza kuti apeze chipambano mmasewerowa.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 1-1 pa bwalo la Kamuzu ndipo wati timu yake inaunikira momwe Wanderers imafooka kuti achite bwino ndipo pang'onong'ono zikanathekadi.
"Tinakhala pansi nkuyang'ana momwe amafooka, munaonanso chigoli China goloboyi wawo amafuna anyadepo ife kungopezapo chigoli, inapeza mipata yoti tikanatha kupambana koma zavuta." Anatero Ikwanga.
Iye anati timu yake yafananitsa mphamvu kwambiri mu ligi mpake amafuna atapeza chipambano koma kuti nayo Wanderers inachita mphamvu ndi kuwabwenzera chigoli pomwe Andrew Joseph anatsogoza Chitipa ndipo Blessings Singini anabwenza.
Timuyi ili pa nambala 11 ndi mapointsi 16 pa zipambano zitatu, kufanana mphamvu kasanu ndi kawiri ndi kugonja kanayi mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores