Malipoti akuonetsa kuti timu ya Blue Eagles ikukonza zolembera bungwe la Supa ligi of Malawi pofuna kuti awunikire ndikuchotsa kadi lachikasu lachiwiri lomwe goloboyi wawo, Joshua Waka anapatsidwa masewero a timuyi ndi FCB Nyasa Big Bullets atatha sabata yangothayi.
Oyimbira Mwayi Msungama anapereka kadi yachikasu kwa Waka yemwe anapita kukakwera golo ngati chisangalalo pomwe Blue Eagles inagonjetsa Bullets 0-1 pa bwalo la Kamuzu.
Waka wakhala akuchita izi kwa masewero angapo potengeranso ndi zomwe zimachitika mmayiko ena pomwe osewera amatha kukwera pagolo masewero akatha kuli kusangalala.
Iye anali atapatsidwa kale kadi lina lachikasu Kamba kochedwetsa mpira ndipo lachiwirili analandira nalo kadi yofiyira kuonetsa kuti mmasewero akudzawa iyeyu sapezeka pagolo pa timuyi.
Inu mukuona kuti chifukwacho chinakwana kulandira kadi?
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores