Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yalengeza kuti katswiri watimu ya amayi yawo, Tendai Sani wachotsa kutimuyi pomwe amugulitsa kutimu ya ZISD yomwe imasewera mu ligi ya amayi yaku Zambia.
Katswiriyu anapita kutimuyi pomwe inali Blantyre Zero mu 2022 ndipo wakhala wofunikira kwambiri pomwe amagoletsa zigoli kutimuyi.
Uyu ndi osewera Wachiwiri mu sabata ino kulowera mmayiko a kunja kutsatira kuchokanso kwa Faith Chimzimu kupita ku timu ya FC Hacken kuchokera ku Ascent Academy.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores