"Tisake osewera ena mwina nkupezako ngati Mwalilino" - Kaunda
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Oscar Kaunda, wati timu yake ilowa pa msika kuti isakeko osewera omwe alimbitse timuyi komanso kumagoletsa ngati amachitira Blessings Mwalilino.
Iye amayankhula atatha masewero omwe apambana 1-0 ndi timu ya Creck Sporting Club kuti atolereko ma points atatayaxbk oochuluka masewero asanu apitawa.
Iye anali okondwa kutsatira kupambanako ndipo anati timu yake inapanikiza kwambiri pomwe Creck simaopsa komabe akhale akulimbitsa timu yawo chigawo choyamba chikatha.
"Tikuyenera kusaka osewera awiri atatu kuti athandize kulimbitsa anawa, tiyenera kupita pa msika mwina tingapezeko ngati achina Blessings Mwalilino nde tiyang'ana mu National Division Ligi umu." Anatero Kaunda.
Timuyi ili pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) pomwe yatolera ma points 20 pa zipambano kasanu ndi kamodzi (6), kulepherana kawiri ndi kugonja kasanu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores