"Tikayesetsa kuti tikamenye bwino kuti tikapeze chipambano." - Msakakuona
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, De Klerk Msakakuona, wati masewero pakati pa timu yake ndi FCB Nyasa Big Bullets amakhala ovuta kwambiri akakumana ndipo anthu akaonera masewero abwino lamulungu pomwe akayesetse kuti apambane.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe alipo pa bwalo la Kamuzu lamulungu masana ndipo wati Bullets ndi timu yabwino koma akayesetsa kuti achite bwino.
"Matimuwa akakumana umakhala mpira wovuta kwambiri moti zotsatira zimadziwika pa mapeto a masewero koma takonzeka bwino ndipo tionetsetsa kuti tidzasewere bwino kuti tidzapambane." Anatero Msakakuona.
Iye wati timu yake ilibe osewera aliyense yemwe ali wovulala ndipo zangokhala kutimuyi kuti adzasankhe osewera omwe adzasewere masewerowa.
Blue Eagles ili ndi mapointsi 20 omwe awapeza pa masewero asanu, kufanana mphamvu kasanu komanso kugonja kawiri mu ligiyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores