"Zinthu zativuta basi lero" - Abambo
Mkulu woyang'anira aphunzitsi kutimu ya Mighty Tigers, Robin 'Abambo' Alufandika, wati timu yake sinasewere bwino kuposa MAFCO mpake yagonja koma ayesetsa kukonza zinthu kuti ziyambe kuyenda.
Iye amayankhula kutsatira kugonja 3-1 pa bwalo la Chitowe masana a loweruka ndipo anati MAFCO imayenera kupambana pakuti inaseweranso bwino.
"Zativuta tivomereze anzathu asewera bwino kuposa ifeyo nde sitingathe kukamba zambiri tingowafunira zabwino." Iye Anafotokoza.
Iye watinso tsogolo la timuyi ndi labwinobwino pakuti masewero oti asewere ndi ochuluka kwambiri ndipo ayesetsa kuonetsetsa kuti azichita bwino.
Timuyi ili pa nambala 11 mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 10 pa masewero 10 omwe yasewera pomwe yapambana katatu ndi kufanana mphamvu kamodzi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores