"Anyamata ambiri ligi yawakulira" - Nyambose
Mphunzitsi watimu ya Songwe Border United, Christopher Nyambose, wati akamati nzeru za ligi zikuwachepera anyamata ake sikunyoza Koma kuti timuyi ikufunikira kukonzanso kuti iyambe kuchita bwino.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 4-0 ndi timu ya Chitipa United pa bwalo la Karonga ndipo anati osewera ambiri ligiyi yawakulira.
"Anali anyamata omwewa omwe ku ligi yaing'ono amamenya bwino koma tsopano apa zikuvuta. Sitikusiyana ndi osewera a Chitipa Koma nzeru ndi zomwe zikuvuta, sikuti onse ndi oipa Koma kuli ena oti tidzayambira kumangira pamenepo." Anatero Nyambose.
Iye wati pagolo pawo ndi pabwino, ena kumbuyo kwawonso ndi abwino ndipo pakati pawo palinso bwino koma kutsogolo kwawo ndi koferatu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores