"Tikakangopusa nafe akatichinya" - Chatama
Mphunzitsi watimu ya Ekhaya FC, Enos Chatama, wati sakuyenera kuyipeputsa timu ya Mzuzu City Hammers poti timu iliyonse mu ligi ndi yovuta kwambiri koma akonzekera kuti akachite bwino.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe aliko lamulungu pa bwalo la Rumphi ndipo wati akachilimika kuti akachite bwino Koma sakuyipeputsa Hammers.
"Timu iliyonse ndi yovuta mu ligi oti ngakhale itagonja kochuluka imatha kupambana nthawi ina nde ifenso titati tapusa adzatimenya." Anatero Chatama.
Iwe wati osewera omwe ali nawo ndi okwana bwino ndipo sakuchita mantha poti akusewera koyenda poti kusewera mpira ndi kumodzi.
Timuyi ili pa nambala yachitatu mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 16 pa masewero 8 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores