"Angakhale K50 tilandira tavutika" - Abambo
Mkulu woyang'anira aphunzitsi kutimu ya Mighty Tigers, Robin 'Abambo' Alufandika, wati timu yawo ili mmavuto azachuma ndipo wapempha makampani ndi anthu akufuna kwabwino kuti athandize timuyi.
Iye anayankhulapo pomwe amatsimikiza kuti timuyi sinalandire K20 million kuchokera ku bungwe la Super League of Malawi komanso Football Association of Malawi zomwe matimu amapatsidwa pachiyambi pa ligi ya TNM.
Iye anakana kuthilirapo mlomo pa nkhaniyi koma wanenapo kuti ngati timu yawo ikuvutika kwambiri.
"Ngati pali ena omwe amatha kufikira makampani atithandize tiwalembere kuti tipeze thandizo kapena munthu atha kututhandiza chifukwa tikamati Maite zonse zimayenda ndi makobidi." Anafotokoza Abambo.
Iwo ati ndalama iliyonse Ali ololera kulandira bola igwire ntchito yoyenerera kutimuyi.
Tigers ilibe wowathandiza kutsatira kutha mgwirizano ndi kampani ya Wakawaka yomwe inangowapatsa unifolomu chaka chino ngakhala mgwirizano unatha.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores