"Tsogolo la Songwe ndi lowala" - Nyambose
Mphunzitsi watimu ya Songwe Border United, Christopher Nyambose, wati palibe timu imene ifike mapointsi 63 mu ligi ndipo masewero 21 omwe atsala nawo ndi ochuluka kwambiri kuti timuyi sidzatuluka mu ligi.
Iye amayankhula atagonja 3-0 ndi timu ya Premier Bet Dedza Dynamos lamulungu pa bwalo la Dedza ndipo wati osewera atimuyi alibe nzeru zosewerera mu supa ligi mpake zikuwavuta.
"Tsogolo ndi lowala la Songwe chifukwa masewero atsala ambiri, 21 ndekuti ndi mapointsi 63 nde ndikukayikira kuti olo timu yotenga ligi idzafika mapointsi amenewa nde timenyabe nkhondo." Anatero Nyambose.
Iye watinso timuyi ikhale ikusaina osewera owonjezera kutimuyi kuti alimbitse timuyi poti ilibe osewera omwe atha kumapeza zigoli kutimuyi.
Songwe ikadali pa nambala 16 mu ligi pomwe ili ndi point imodzi pa masewero asanu ndi anayi mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores