"Apa tsopano ligi yayamba" - Mwakhwawa
Mphunzitsi wa timu ya Baka City, Victor Mwakhwawa wati ndi wokondwa poti wachepetsa mpata wa iwo ndi timu ya Mitundu Baptist mu NBS Bank National Division League ndipo tsopano ligi yayamba.
Iye amayankhula atatha masewero omwe timu yake inagonjetsa Baptist 1-0 kuti ifike pa nambala yachiwiri mu ligiyi komanso kukhala oyamba kugonjetsa Mitundu mu ligiyi.
Iye anali wokondwa kwambiri ndi chipambanochi ndipo anati anagwiritsa ntchito nzeru zokuya kuti apambane mmasewerowa.
"Anali masewero ovuta kwambiri chifukwa anzathuwa anali asanagonjepo nde tinaona mmene akhala akuchitira mmbuyomu amagoletsa kwambiri nde tinayika osewera ambiri pakati. Apa tachepetsa mpata pa iwo ligi yayamba lero." Anatero Mwakhwawa.
Timuyi ili tsopano ili pa nambala yachiwiri ndi mapointsi asanu ndi atatu pa masewero anayi omwe yasewera ndipo yapamwamba kawiri ndi kufanana mphamvu kawiri.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores