TN STARS YABWERERA MU CHIPIKU
Timu yomwe inasewerapo mu ligi ya TNM Supa ligi Kuchokera mu chaka cha 2019 mpaka 2022, TN Stars, isewera mu ligi ya Chipiku Stores Premier Division chaka chino kutsatira kuchita bwino mu masewero achipulula.
Izi zikutsatira kuchita bwino pa masewero achipulula omwe timuyi inakwanitsa kugonjetsa Dwangwa United 1-0 isanagonjetsenso LUANAR FC 1-0 kuti ichoke mu ligi ya Division One.
Bungwe loyendetsa mpira mchigawo chapakati latulutsa ndandanda wa matimu 16 omwe asewere mu mpikisanowu wa chaka chino ndipo matimuwa ndi Airborne Rangers, Armour Battalion, Blue Eagles Reserve, Chatoloma ADMARC, Chisomo Academy, Dwangwa United, Ekas Freight Wanderers, Extreme FC, Green Rangers, Santhe ADMARC, Silver Strikers Reserves, Mchinji Boma Stars, Mbabzi United, TN Stars, Panthers FC komanso Wimbe United.
Bungweli latinso matimu adzakumana ina ndi inzake potolera mapointsi mu masewero 30 kusiyana ndi mmbuyomu momwe matimu amagawidwa mmagulu.
TN Stars inatuluka mu Sup