Manda: Ndine wokondwa popita ku Wanderers
Katswiri watsopano wa Mighty Wanderers, Masiya Manda, wati ndi wosangalala kwambiri kamba koti wapita kutimuyi poti ndi khumbo la osewera ochuluka kupita ku timu yaikulu.
Iye amayankhula atatha kusaina mgwirizano wa zaka zitatu ndi timuyi loweruka masana ndipo wati akufuna ayithandize timuyi ndi zimene amatha kale.
"Ndiyesetsa kupereka zomwe ndimadziwazo komanso kuthandizana ndi anzanga omwe aliko kale kuti tizichita bwino." Anatero Manda.
Ndipo mphunzitsi watimuyi, Bob Mpinganjira, wati timuyi inafunitsitsa Manda poti mmodzi mwa osewera abwino mdziko muno.
"Tili ndi osewera ena pa malo omwe amasewerapo koma kubwera kwake kubwera mpikisano pa osewera akumbuyo." Anatero Mpinganjira.
Manda anali ku Mighty Tigers chaka cha 2023 ndipo chaka chatha anapita ku Civil Service United komwe anachitanso bwino Kwambiri.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores