"Aja mukuti sanagonje aja akudalira wa kutsogolo wathu" - Kaunda
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Oscar Kaunda, wati timu yake ndi ya osewera achisodzera ndi chifukwa chake amasowekera ukadaulo mmalo ena pa masewero omwe agonja 1-2 ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets mu chikho cha Airtel Top 8.
Iye anayankhulapo atatha masewerowa kuti atuluke mu chikhochi ndipo anavomereza kugonja kwawo poyifunira zabwino Bullets kuti yafika mu ndime ina.
Iye anayamikiranso osewera ake kuti anasewera bwino koma poti ndi timu yatsopano, ukadaulo wina akadaphunzira.
"Ndi zoona ukadaulo wina ukufunika Koma timuyi tikuumba kumene nde ana wa akadaphunzira nde timati tikaumba ena amatitengera. Aja mukuti sanagonje aja akudaliranso wa ife nde timati tikakonza amatitengera momwemo basi." Anatero Kaunda.
Iyenso wati kusewera usiku sikunapange Kalikonse pa masewero awo poti iwo sanadandauleko za usiku ndiponso asewera bwinobwino.
"Ife ngati osewera ndi aphunzitsi mbali yathu sitinadandauleko za kusewera
0992439790
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores