"Ngati ukuyenera kukhala Katswiri ukuyenera kugonjetsa akatswiri" - Mpulula
Mphunzitsi watimu ya Mighty Tigers, Leo Mpulula, wati timu yake ikudziwa kuti FCB Nyasa Big Bullets ibwera mokwiya poti ikuchokera kogonja koma aonetsetsa kuti pakutha tsiku la lero apeze chipambano.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe aliko pa bwalo la Kamuzu lamulungu masana ndipo wati timu yake inapuma mu sabata imodzi yomwe sinasewereyi zomwe zawathandiza kuti osewera ovulala achire.
"Akhala masewero ovuta kwambiri kutengera kuti Bullets ikuchokera kogonja nde ikabwera kuti ipeze chigoli cha chamsanga koma takonza zolakwika zathu kuti pakutha pa tsiku tipeze mapointsi abwino." Iye Anafotokoza.
Timu ya Tigers ili pa nambala yachikhumi mu ligi ndi mapointsi khumi pa masewero asanu ndi atatu omwe asewera.
0991509953
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores