Mphunzitsi watimu ya Flames Marian Mario Marinica wasankha Patrick Mabedi komanso Franco Ndawa ngati aphunzitsi omuthandizira pa ntchito yake.
Awiri-wa akuyembekezeka kugwira ntchito ndi Marinica pamene timu ya Flames ikuyamba zokonzekera zake kumathero a sabata ino.
Malingana ndi Marinica, Enos Chatama komanso Peter Mgangira akhalanso akumuthandiza pa ntchitoyi komanso kuphunzira zina ndi zina.
Kupatula awiri-wa, mphunzitsi watsopano wa Flames-yu wasankha James Sangala kuti azipereka ukadaulo kwa aphunzitsi omwe akugwira naye ntchito.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores