"Ndikusangalala ndi momwe ligi ikuyendera" - Kaunda
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Oscar Kaunda, wati ligi ya chaka chino ikuyenda bwino kwambiri poti matimu akumatha kumakagonjetsa anzawo koyenda zomwe zikuonetsa kuti pali mpikisano.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 0-1 ndi timu ya Blue Eagles kuti akhale masewero anayi otsogozana osapezako chipambano mu ligi.
Iye anati timu yake ikuphunzira ochuluka ndi momwe ligi ikuyendera ndipo mchigawo chachiwiri adzabwera mwa mphamvu kwambiri.
"Ligi ikuyenda bwino kwambiri ngati achina Blue Eagles akumabwera kudzatichinya kuno kenako ifenso tikumachinya ena ndekuti mpikisano ulipo kwambiri." Anatero Kaunda.
Komabe iye anadandaulapo za oyimbira yemwe anati anawakanira chigoli chooneka bwinobwino mmasewerowa Koma avomereza.
Timuyi ili pa nambala yachisanu ndi chiwiri (7) ndi mapointsi okwana 17 pa masewero okwana 12 atapeza zipambano zisanu, kufanana mphamvu kawiri ndi kugonja kasanunso mu ligi.
Tipepese kuti zotsatira za Chatoloma Admarc vs Extreme tazipeza lero, inatha 1-1 dzulo. Izi zapangitsa kuti nambala ya olosera apa top 4 itsike kuchoka pa 38 kufika pa 25. PEPANI KWAMBIRI 🙏
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores