"TINAPEMPHA KUTI TISEWERE LACHITATU" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Creck Sporting Club, Eliya Kananji, wati timu yake inapempha kuti isewere lachitatu ndi Silver Strikers cholinga choti apume poti anangopuma tsiku limodzi atasewera ndi Mighty Wanderers mu chikho cha FDH Bank.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-1 ndi Silver Strikers pa bwalo la Silver pomwe anayamikira kuti anyamata ake anachita bwino koma anakambapo nkhani ya kutopa kwa osewera ake.
"Tinasewera lamulungu ndi Wanderers pa masewero aakulunso nde tinapempha kuti mwina tisewere lachitatu koma sanatimve nde tinangotsatira poti timangouzidwa," anatero Kananji.
Iye wadandaulanso ndi kuvulalavulala kwa osewera a timu yake pomwe wati mbali ina ya timu ikumakanika kugwirana kupangitsa kuti azivutika mmasewero ena komabe wati timu yake tsopano ikulimbitsa mtima ndipo mmasewero omwe atsala nawo achita bwino.
Creck ili pa nambala 10 mu ligi ndi mapointsi 25 pa zipambano 6, kulepherana ka 7 ndi kugonja ka 8.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores