TAYIPHA EQUATORIAL GUINEA MOPHWEKA
Bungwe la Confederations of African Football (CAF) lapereka ma points atatu komanso zigoli zitatu kutimu ya dziko lino kuti yagonjetsa timu ya Equatorial Guinea 3-0.
Watsimikiza nkhaniyi ndi Mkulu woona za mpikisano ku bungwe la Football Association of Malawi, Gomegzani Zakazaka, kutsatira uthenga womwe CAF yatumiza.
Izi zikudza kutsatira kuti timu ya Equatorial Guinea yakanika kufika m'dziko muno kamba koti osewera a mdzikolo sakumvana ndi bungwe loyendetsa mpira m'dziko lawolo.
Ndipo pofuna kungosangalatsa maso, timu ya Flames yagawana pakati pomwe ikhale ndi masewero ongogiligishana nthawi ya 6 koloko madzulo ano.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores